Nena ndi nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, cokonda m'maso mwanu, cimene moyo wanu ali naco cifundo; ndipo ana anu amuna ndi akazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.