8. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
9. Wobadwa ndi munthu iwe, nenera ndi kuti, Atero Yehova, Nena, Lupanga, lupanga lanoledwa, latuulidwanso;
10. lanoledwa kuti liphetu, lituulidwa kuti linge mphezi; tisekererepo kodi? ndilo ndodo yacifumu ya mwana wanga, yopeputsa mtengo uli wonse.
11. Ndipo analipereka alituule, kuti acite nalo lupangali analinola, inde analituula kulipereka m'dzanja la wakupha.