Ezekieli 21:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Yerusalemu, nuwabenthulire mau malo opatulikawa, nunenere dziko la Israyeli kulitsutsa;

3. nuziti kwa dziko la Israyeli, Atero Yehova, Taona Ine ndine wotsutsana nawe, ndidzasolola lupanga langa m'cimace, ndi kukulikhira olungama ndi oipa.

4. Popeza ndidzakulikhira olungama ndi oipa, cifukwa cace lupanga langa lidzasololokera anthu onse, kuyambira kumwera kufikira kumpoto;

5. ndi anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndasolola lupangalanga m'cimace, silidzabwereranso.

Ezekieli 21