5. Cinatengakonso mbeu ya m'dziko, ndi kuibzala m'nthaka yokoma, cinaiika panali madzi ambiri, cinaioka ngati mtengo wamsondodzi.
6. Ndipo inaphuka, nikhala mpesa wotambalala wofupi msinkhu, nthambi zace zinapindikira momwe, ndi mizu yace pansi pace, nikhala mpesa, nuonetsa nthambi ndi kuphuka mphukira.
7. Panalinso ciombankhanga cina cacikuru, ndi mapiko akuru, ndi nthenga zambiri; ndipo taona, mpesa uwu unacipindira mizu yace, nucilunjikitsira nthambi zace, kucokera pookedwa pace, kuti ciuthirire madzi.