Ezekieli 17:13-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. nitenga wa mbumba yacifumu, nicita naye pangano, nimlumbiritsa, nicotsa amphamvu a m'dziko;

14. kuti ufumuwo ukhale wopepuka, kuti usadzikweze, koma kuti pakusunga pangano lace ukhale.

15. Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yace ku Aigupto, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? adzapulumuka wakucita izi? atyole pangano ndi kupulumuka kodi?

16. Pali Ine, ati Ambuye Yehova, pamalo pokhala mfumu, imene idamcititsa ufumu, imene anapeputsa lumbiro lace, imene anatyola pangano lace, adzafa pamodzi ndi iye pakati pa Babulo.

Ezekieli 17