Ezara 8:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Wa ana a Yoabu, Obadiya mwana wa Yehieli; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri mphambu khumi kudza asanu ndi atatu.

10. Ndi wa ana a Selomiti, mwana wa Yosifiya; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi.

11. Ndi wa ana a Bebai, Zekariya mwana wa Bebai; ndi pamodzi naye amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu.

12. Ndi wa ana a Azigadi, Yohanana mwana wa Hakatana; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu khumi limodzi.

13. Ndi a ana otsiriza a Adonikmnu, maina ao ndiwo Elifeleti, Yeueli, ndi Semaya; ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi limodzi.

14. Ndi wa ana a Bigivai, Utai ndi Zabudi, ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi awiri.

15. Ndipo ndinawasonkhanitsa ku mtsinje wopita ku Ahava, ndi komweko tinakhala m'misasa masiku atatu; ndipo ndinapenyerera anthu ndi ansembe, koma sindinapezapo wa ana a Levi.

16. Pamenepo ndinatumiza munthu kuitana Eliezere, Ariyeli, Semaya, ndi Elimatana, ndi Natani, ndi Zekariya, ndi Mesulamu, ndiwo akuru; ndi Yoyaribi ndi Elinatani, ndiwo aphunzitsi.

17. Ndipo ndinawatumiza kwa Ido mkuru, ku malo dzina lace Kasifiya; ndinalooganso m'kamwa mwao mau akunena kwa Ido, ndi kwa abale ace Anetini, pa malo paja Kasifiya, kuti azibwera nao kwa ife otumikira za nyumba ya Mulungu wathu.

Ezara 8