6. Ndi wa ana a Adini, Ebedi mwana wa Yonatani; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu.
7. Ndi wa ana a Elamu, Yesaya mwana wa Ataliya; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi awiri.
8. Ndi wa ana a Sefatiya, Zebadiya mwana wa Mikaeli; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi atatu.
9. Wa ana a Yoabu, Obadiya mwana wa Yehieli; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri mphambu khumi kudza asanu ndi atatu.
10. Ndi wa ana a Selomiti, mwana wa Yosifiya; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi.
11. Ndi wa ana a Bebai, Zekariya mwana wa Bebai; ndi pamodzi naye amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu.
12. Ndi wa ana a Azigadi, Yohanana mwana wa Hakatana; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu khumi limodzi.
13. Ndi a ana otsiriza a Adonikmnu, maina ao ndiwo Elifeleti, Yeueli, ndi Semaya; ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi limodzi.
14. Ndi wa ana a Bigivai, Utai ndi Zabudi, ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi awiri.
15. Ndipo ndinawasonkhanitsa ku mtsinje wopita ku Ahava, ndi komweko tinakhala m'misasa masiku atatu; ndipo ndinapenyerera anthu ndi ansembe, koma sindinapezapo wa ana a Levi.
16. Pamenepo ndinatumiza munthu kuitana Eliezere, Ariyeli, Semaya, ndi Elimatana, ndi Natani, ndi Zekariya, ndi Mesulamu, ndiwo akuru; ndi Yoyaribi ndi Elinatani, ndiwo aphunzitsi.