35. Otengedwa ndende, ataturuka m'ndende, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israyeli, ng'ombe khumi ndi ziwiri za Aisrayeli onse, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi imodzi, ana a nkhosa makumi asanu ndi awiri mphambu asanu ndi awiri, atonde khumi ndi awiri, akhale nsembe yazolakwa; zonsezi ndizo nsembe yopsereza ya kwa Yehova.
36. Ndipo anapereka malamulo a mfumu kwa akazembe a mfumu, ndi kwa ziwanga, tsidya lino la mtsinjewo; ndipo iwo anathandiza anthu ndi nyumba ya Mulungu.