Ezara 6:19-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo ana a ndende anacita Paskha tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi woyamba.

20. Pakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa pamodzi, anayera onsewo, naphera Paskha cifukwa ca ana onse a ndende, ndi abale ao ansembe, ndi iwo okha.

21. Ndipo ana a Israyeli obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kucokera conyansa ca amitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israyeli, anadza,

22. nasunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi cimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asuri, kulimbitsa manja ao mu nchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israyeli.

Ezara 6