6. Zolembedwa m'kalata amene Tatinai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setara Bozenai, ndi anzace Afarisikai, okhala tsidya lino la mtsinje, anatumiza kwa Dariyo mfumu,
7. anatumiza kalata kwa iyeyo m'menemo munalembedwa motere, Kwa Dariyo mfumu, mtendere wonse.
8. Adziwe mfumu kuti ife tinamuka ku dziko la Yuda, ku nyumba ya Mulungu wamkuru, yomangidwa ndi miyala yaikuru, niikidwa mitengo pamakoma, nicitika mofulumira nchitoyi, nikula m'dzanja mwao.
9. Pamenepo tinafunsa akulu aja ndi kutere nao, Anakulamulirani ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?
10. Tinawafunsanso maina ao, kukudziwitsani, kuti tilembere maina a anthu akuwatsogolera.