15. nati naye, Tenga zipangizo izi, kaziike m'Kacisi ali m'Yerusalemu, nimangidwe nyumba ya Mulungu pambuto pace.
16. Pamenepo anadza Sezibazara yemweyo namanga maziko a nyumba ya Mulungu iri m'Yerusalemu; ndipo kuyambira pomwepo kufikira tsopano irimkumangidwa, koma siinatsirizike.
17. Ndipo tsono cikakomera mfumu, munthu asanthule m'nyumba ya cuma ca mfumu iri komwe ku Babulo, ngati nkuterodi, kuti Koresi mfumu analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu ku Yerusalemu; ndipo mfumu ititumizire mau omkomera pa cinthuci.