Ezara 5:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Koma makolo athuwo atautsa mkwiyo wa Mulungu wa Kumwamba, Iye anawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo Mkasidi, amene anaononga nyumba yino, natenga anthu ndende kumka nao ku Babulo.

13. Koma caka coyamba ca Koresi mfumu ya Babulo, Koresi mfumuyo analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu.

14. Ndiponso zipangizo za golidi ndi siliva za nyumba ya Mulungu, anaziturutsa Nebukadinezara m'Kacisi anali ku Yerusalemu, ndi kubwera nazo ku kacisi wa ku Babulo, izizo Koresi mfumu anaziturutsa m'kacisi wa ku Babulo, nazipereka kwa munthu dzina lace Sezibazara, amene anamuika akhale kazembe;

15. nati naye, Tenga zipangizo izi, kaziike m'Kacisi ali m'Yerusalemu, nimangidwe nyumba ya Mulungu pambuto pace.

Ezara 5