Estere 9:13-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Nati Estere, Cikakomera mfumu, alole Ayuda okhala m'Susani acite ndi mawa lomwe monga mwa lamulo la lero; ndi ana amuna khumi a Hamani apacikidwe pamtengo.

14. Ndipo mfumu inati azicita motero, nalamulira m'Susani, napacikidwa ana amuna khumi a Hamani.

15. Ndipo Ayuda okhala m'Susani anasonkhana pamodzi, tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi wa Adara, napha amuna mazana atatu m'Susani; koma sanalanda zofunkha.

16. Nasonkhana pamodzi Ayuda ena okhala m'maiko a mfumu, nalimbikira moyo wao, napumula pa adani ao, nawapha a iwo odana nao zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu; koma sanalanda zofunkha.

17. Cinacitika ici tsiku lakhumi ndi citatu la mwezi wa Adara, ndi tsiku lace lakhumi ndi cinai anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwesa.

18. Koma Ayuda okhala m'Susani anasonkhana tsiku lace lakhumi ndi citatu ndi lakhumi ndi cinai, ndi pa tsiku lakhumi ndi cisanu anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera.

19. Cifukwa cace Ayuda a kumiraga, okhala m'midzi yopanda malinga, amaliyesa tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi wa Adara tsiku la kukondwera ndi madyerero, ndi tsiku lokoma, ndi lakutumizirana magawo.

20. Ndipo Moredekai analembera izi, natumiza akalata kwa Ayuda onse okhala m'maiko onse a mfumu Ahaswero, a kufupi ndi a kutali,

21. kuwalimbikitsira, asunge tsiku lakhumi ndi cinai, mwezi wa Adara, ndi tsiku lace lakhumi ndi cisanu lomwe, caka ndi caka,

22. ndiwo masiku amene Ayuda anapumula pa adani ao; ndi mwezi wacisoni unawasandulikira wakukondwera, ndi wamaliro ukhale tsiku lokoma, awayese masiku amadyerero ndi akukondwera, akutumizirana magawo, ndi akupatsa zaufulu kwa osauka.

23. Ndipo Ayuda anabvomereza kucita monga umo adayambira, ndi umo Moredekai adawalembera;

24. popeza Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda onse, adapangira Ayuda ciwembu kuwaononga, naombeza Puri, ndiwo ula, kuwatha ndi kuwaononga;

Estere 9