14. Naturuka amtokoma okwera pa akavalo aliwiro acifumu; pakuti mau a mfumu anawafulumiza ndi kuwaumiriza; ndipo lamulolo linabukitsidwa m'cinyumba ca ku Susani.
15. Ndipo Moredekai anaturuka pamaso pa mfumu wobvala cobvala cacifumu camadzi ndi coyera, ndi korona wamkuru wagolidi, ndi maraya abafuta ndi ofiirira; ndi mudzi wa Susani unapfuula ndi kukondwera.
16. Ayuda anali nako kuunika, ndi kukondwera, ndi cimwemwe, ndi ulemu.
17. Ndi m'maiko monse, ndi m'midzi yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lace, Ayuda anali nako kukondwera ndi cimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m'dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera.