13. Ndipo anatumiza akalata ndi amtokoma ku maiko onse a mfumu, kuti aononge, aphe, napulule Ayuda onse, ndiwo ana, ndi okalamba, makanda, ndi akazi, tsiku limodzi, ndilo tsiku lakhumi ndi citatu la mwezi wakhumi ndi ciwiri, ndiwo mwezi wa Adara; nalande zao mofunkha.
14. Mau a colembedwaco, ndiwo kuti licitike lamulo m'maiko onse, analalikidwa kwa anthu onse, kuti akonzekeretu tsiku lomwelo.
15. Amtokoma anaturuka ofulumizidwa ndi mau a mfumu, ndi lamulo linabukitsidwa m'cinyumba ca ku Susani; ndipo mfumu ndi Hamani anakhala pansi kumwa; koma mudzi wa Susani unadodoma.