Estere 2:19-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo posonkhanidwa anamwali nthawi yaciwiri Moredekai anali wa m'bwalo la mfumu.

20. Estere sadaulula cibale cace kapena mtundu wace, monga Moredekai adamuuza; popeza Estere anacita mau a Moredekai monga m'mene analeredwa naye.

21. Masiku awa pokhala Moredekai wa m'bwalo la mfumu, Bigitana ndi Teresi, adindo awiri a mfumu osunga pakhomo, anapsa mtima, nayesa kumthira manja mfumu Ahaswero.

22. Koma cidadziwika ici kwa Moredekai, ndiye anafotokozera Estere mkazi wamkuru; ndi Estere anamuuza mfumu, kumnenera Moredekai.

23. Ndipo atafunsira mlanduwo, anaupeza momwemo, napacikidwa onse awiri pamtengo; ndipo anacilemba m'buku la mbiri pamaso pa mfumu.

Estere 2