Estere 10:2-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndi zocita zonse za mphamvu yace, ndi nyonga zace, ndi mafotokozedwe a ukulu wa Moredekai, umene mfumu inamkulitsa nao, sizilembedwa kodi m'buku la mbiri ya mafumu a Mediya ndi Perisiya?

3. Pakuti Moredekai Myuda anatsatana naye mfumu Ahaswero, nakhala wamkuru mwa Ayuda, nabvomerezeka mwa unyinji wa abale ace wakufunira a mtundu wace zokoma, ndi wakunena za mtendere kwa mbeu yace yonse.

Estere 10