20. Ndipo Mose ndi Aroni anacita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m'nyanjamo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ace; ndipo madzi onse a m'nyanjamo anasanduka mwazi.
21. Ndi nsomba za m'nyanjamo zinafa; ndi nyanjayo inanunkha; ndipo Aaigupto sanakhoza kumwa madzi a m'nyanjamo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Aigupto.
22. Ndipo alembi a Aigupto anacita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvera iwo; monga adalankhula Yehova.