Eksodo 40:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lazolidi cakuno ca likasa la mboni, numange pakacisi nsaru yotsekera pakhomo.

6. Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la kacisi wa cihema cokomanako.

7. Ukaikenso mkhate pakati pa cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.

8. Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupacika nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo.

9. Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nao kacisi, ndi zonse ziri m'mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zace zonse; ndipo adzakhala wopatulika.

10. Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zace zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulikitsa.

11. Udzozenso mkhate ndi tsinde lace, ndi kuupatula.

12. Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ace amuna ku khomo la cihema cokomanako, ndi kuwasambitsa ndi madzi.

Eksodo 40