Eksodo 40:16-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anacita.

17. Ndipo kunali, mwezi woyamba wa caka caciwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa kacisi.

18. Ndipo Mose anautsa kacisi, nakhazika makamwa ace, naimika matabwa ace, namangapo mitanda yace, nautsa mizati ndi nsanamira zace.

19. Ndipo anayalika hema pamwamba pa kacisi, naika cophimba ca cihema pamwamba pace; monga Yehova adamuuza Mose.

20. Ndipo anatenga mboniyo, naiika mlikasa, napisa mphiko palikasa, naika cotetezerapo pamwamba pa likasa;

21. nalowa nalo likasa m'kacisi, napacika nsaru yocinga, nacinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose.

22. Ndipo anaika gomelo m'cihema cokomanako, pa mbali ya kumpoto ya kacisi, kunja kwa nsaru yocinga.

23. Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

24. Ndipo anaika coikapo nyali m'cihema cokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwela ya kacisi.

Eksodo 40