Eksodo 4:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Mose anayankha nati, Koma taonani, sadzakhulupirira ine, kapena kumvera mau anga; pakuti adzanena, Yehova sanakuonekera iwe.

2. Ndipo Yehova ananena naye, Ico nciani m'dzanja lako? Nati, Ndodo.

3. Ndipo ananena iye, Iponye pansi. Naiponya pansi, ndipo inasanduka njoka; ndipo Mose anaithawa.

Eksodo 4