1. Ndipo anaomba zobvala zakutumikira nazo ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, atumikire nazo m'malo opatulika, naomba zobvala zopatulika za Aroni; monga Yehova adamuuza Mose.
2. Ndipo anaomba efodi wa golidi, lamadzi, lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
3. Ndipo anasula golidi waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya mmisiri.
4. Anapangira efodi zapamapewa zolumikizana; pa nsonga ziwirizo anamlumikiza.