6. Napanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi mkuwa.
7. Ndipo anapisa mphikozo m'zimphetemo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere.
8. Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lace lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la cihema cokomanako.
9. Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwela, kumwela, nsaru zocingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;
10. nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace zasiliva.