Eksodo 37:24-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Anacipanga ici ndi zipangizo zace zonse za talente wa golidi woona.

25. Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wasitimu; utali wace mkono, ndi kupingasa kwace mkono, lampwamphwa; ndimsinkhu wace mikono iwiri; nyanga zace zinaturuka m'mwemo.

26. Ndipo analikuta ndi golidi woona, pamwamba pace, ndi mbali zace pozungulira, ndi nyanga zace; ndipo analipangira mkombero wagolidi pozungulira pace.

Eksodo 37