10. Ndipo anapanga gome la mtengo wasitimu; utali wace mikono iwiri, ndi kupingasa kwace mkono limodzi, ndi msinkhu wace mkono ndi hafu;
11. ndipo analikuta ndi golidi woona, nalipangira mkombero wagolidi pozungulira pace.
12. Analipangiranso mitanda pozungulirapo, yoyesa cikhato m'kupingasa kwace, ndi pamitanda pace pozungulira anapangirapo mkombero wagolidi.
13. Ndipo analiyengera mphete zinai zagolidi, naika mphetezo pa ngondya zace zinai zokhala pa miyendo yace inai.
14. Mphetezo zinali pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko kunyamulira nazo gomelo.
15. Ndipo anapanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndigolidi, kunyamulira nazo gomelo.