Eksodo 36:8-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akucita nchitoyi anapanga kacisi ndi nsaru zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi; ndi lofiira, ndi lofiira, ndi akerubi, nchito ya mmisiri.

9. Utali wace wa nsaru yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwace kwa nsaru imodzi mikono inai; nsaru zonse zinafanana muyeso wao.

10. Ndipo analumikiza nsaru zisanu yina ndi inzace; nalumikiza nsaru zisanu zina yina ndi inzace.

11. Ndipo anaika magango ansaru yamadzi m'mphepete mwace mwa nsaru imodzi ku mkawo wa cilumikizano; nacita momwemo m'mphepete mwace mwa nsaru ya kuthungo, ya cilumikizano caciwiri.

12. Anaika magango makumi asanu pa nsaru imodzi, naikanso magango makumi asanu m'mphepete mwace mwa nsaru ya cilumikizano cina; magango anakomanizana lina ndi linzace.

Eksodo 36