3. Musamasonkha mota m'nyumba zanu ziri zonse tsiku la Sabata.
4. Ndipo Mose ananena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, ndi kuti, Ici ndi cimene Yehova anauza ndi kuti,
5. Mumtengere Yehova copereka ca mwa zanu; ali yense wa mtima womfunitsa mwini abwere naco, ndico copereka ca Yehova;
6. golidi, ndi siliva, ndi mkuwa; ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi;
7. ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wasitimu;
8. ndi mafuta akuunikira, ndi zonunkhira za mafuta odzoza, ndi cofukiza ca pfungo lokoma;
9. ndi miyala yasohamu, ndi miyala yoika ya efodi, ndi ya capacifuwa.