Eksodo 35:17-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. nsaru zocingira za kubwalo, nsici zace, ndi makamwa ace, ndi nsaru yotsekera ku cipata ca pabwalo;

18. ziciri za cihema, ndi ziciri za kubwalo, ndi zingwe zao;

19. zobvala za kutumikira nazo m'maopatulika, zobvala zopatulika za. Aroni wansembe, ndi zobvala za ana ace, zakugwira nazo nchito ya nsembe.

20. Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linacoka pamaso pa Mose.

21. Ndipo anadza, ali yense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wace wamfunitsa, nabwera naco copereka ca Yehova, ca ku nchito ya cihema cokomanako, ndi ku utumiki wace wonse, ndi ku zobvala zopatulika.

22. Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ace, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m'makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zidzingwiri, zonsezi zokometsera zagolidi; inde yense wakupereka kwa Yehova copereka cagolidi.

Eksodo 35