Eksodo 35:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Mose anasonkhanitsa khamu lonse la ana a Israyeli, nanena nao, Siwa mau amene Yehova anauza, kuti muwacite.

2. Masiku asanu ndi limodzi azigwira nchito; koma tsiku lacisanu ndi ciwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: ali yense agwira nchito pamenepo, aphedwe,

3. Musamasonkha mota m'nyumba zanu ziri zonse tsiku la Sabata.

Eksodo 35