4. Ndipo anazilandira ku manja ao, nacikonza ndi cozokotera, naciyenga mwana wa ng'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kucokera m'dziko la Aigupto.
5. Pakuciona Aroni, anamanga guwa la nsembe patsogolo pace; ndipo Aroni anapfuula nati, Mawa aliko madyerero a Yehova.
6. Ndipo m'mawa mwace anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.
7. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kucokera m'dziko la Aigupto wadziipsa;