Eksodo 32:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kupfuula kwa olakika, kapena la kupfuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang'ombe.

19. Ndipo kunali, pamene anayandikiza cigono, anaona mwana wa ng'ombeyo ndi kubvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwace, nawaswa m'tsinde mwa phiri.

20. Ndipo anatenga mwana wa ng'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israyeli.

21. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakucitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukuru kotere?

22. Ndipo Aroni anati, Asapse mtima mbuye wanga; udziwa anthuwa kuti akhumba coipa.

23. Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kucokera m'dziko la Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.

24. Ndipo ndinanena nao, Ali yense ali naye golidi amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinaciponya m'moto, ndimo anaturukamo mwana wa ng'ombe uyu.

Eksodo 32