7. cihema cokomanako, likasa la mboni, ndi cotetezerapo ciri pamwamba pace, ndi zipangizo zonse za cihemaco;
8. ndi gomelo ndi zipangizo zace, ndi coikapo nyali coona ndi zipangizo zace, ndi guwa la nsembe lofukizapo;
9. ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zace zonse, ndi mkhate ndi tsinde lace;
10. ndi zobvala zotumikira nazo, ndi zobvala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zobvala za ana ace, zakucita nazo nchito ya nsembe;
11. ndi mafuta odzoza, ndi cofukiza ca zonunkhira zokoma za malo opatulika; azicita monga mwa zonse ndakuuza iwe.
12. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
13. Koma iwe, lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo cizindikilo pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.