6. Nuliike cakuno ca nsaru yocinga iri ku likasa la mboni, patsogolo pa cotetezerapo ciri pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe.
7. Ndipo Aroni azifukizapo cofukiza ca zonunkhira zokoma m'mawandim'mawa, pamene akonza nyalizo, acifukize.
8. Ndipo pamene Aroni ayatsa nyalizo madzulo, acifukize cofukiza cosatha pamaso pa Yehova mwa mibadwo yanu,
9. Musafukizapo cofukiza cacilendo, kapena nsembe yopsereza, kapena copereka; musathirepo nsembe yothira.
10. Ndipo Aroni azicita coteteza pa nyanga zace kamodzi m'caka; alicitire coteteza ndi mwazi wa nsembe yaucimo ya coteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulikitsa la Yehova.