Pamene uwerenga ana a Israyeli, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova ciombolo ca pa moyo wace, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.