Eksodo 3:21-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo ndidzapatsa anthu awa ufulu pamaso pa anthu a Aigupto; ndipo kudzakhala, pamene muturuka simudzaturuka opanda kanthu;

22. koma mkazi yense adzafunse mnzace, ndi mlendo wokhala m'nyumba mwace, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolidi, ndi zobvala; ndipo mudzabveke nazo ana anu amuna ndi akazi; ndipo mudzafunkhe za Aaigupto.

Eksodo 3