37. Ucitire guwa la nsembe coteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo a guwa la nsembelo likhale lopatulikitsa; ciri conse cikhudza guwa la nsembelo cikhale copatulika.
38. Koma izi ndizo uzikonza pa guwa la nsembelo; ana a nkhosa awiri a caka cimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza.
39. Mwana wa nkhosa wina ukonze m'mawa; ndi mwana wa nkhosa wina ukonze madzulo;
40. ndi pa mwana wa nkhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira.