Eksodo 29:34-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m'mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza ncopatulika ici.

35. Ndipo utero nao Aroni, ndi ana ace amuna, monga mwa zonse ndakuuza; udzaze manja ao masiku asanu ndi awiri.

36. Nukonze ng'ombe yamphongo, ndiyo nsembe yaucimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakucita coteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula.

37. Ucitire guwa la nsembe coteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo a guwa la nsembelo likhale lopatulikitsa; ciri conse cikhudza guwa la nsembelo cikhale copatulika.

38. Koma izi ndizo uzikonza pa guwa la nsembelo; ana a nkhosa awiri a caka cimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza.

39. Mwana wa nkhosa wina ukonze m'mawa; ndi mwana wa nkhosa wina ukonze madzulo;

Eksodo 29