22. Ndipo uzipanga matabwa asanu ndi limodzi kwa mbali ya kacisi ya kumbuyo kumadzulo.
23. Nupange matabwa awiri a ngondya za kacisi za kumbuyo.
24. Ndipo akhale ophatikizika pamodzi patsinde, nakhalenso ophatikizika pamodzi kumutu kwace ndi mphete imodzi; azitero onse awiri; azikhala a ngondya ziwiri.
25. Ndipo pakhale matabwa asanu ndi atatu, ndi makamwa ao asiliva, ndiwo makamwa khumi mphambu asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.
26. Ndipo uzipanga mitanda ya mtengo wasitimu; isanu ya matabwa a pa mbali yina ya kacisi,
27. ndi mitanda isanu ya matabwa a Pel mbali yina ya kacisi, ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ya kacisi ya kumbuyo kumadzulo.
28. Ndi mtanda wa pakati pa matabwa ufikire kuthungo.
29. Ndipo uzikuta matabwa ndi golidi, ndi kupanga mphete zao zagolidi zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golidi.