29. Ndipo uzipanga mbale zace, ndi zipande zace, ndi mitsuko yace, ndi zikho zace zakuthira nazo; uzipanga za golidi woona.
30. Ndipo uziikamkate woonekera pa gomelo pamaso panga nthawi zonse.
31. Ndipo uzipanga coikapo nyali ca golidi woona; coikapoco cisulidwe mapangidwe ace, tsinde lace ow thupi lace; zikho zace, mitu yace, ndi maluwa ace zikhale zocokera m'mwemo;
32. ndipo m'mbali zace muturuke mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za coikapo nyalico zituruke m'mbali yace yina, ndi mphanda zitatu za coikapo nyalico zituruke m'mbali inzace.