Eksodo 24:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo anatenga buku la Cipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzacita, ndi kumvera.

8. Ndipo Mose anatenga mwaziwo, nawaza pa anthu, nati, Taonani mwazi wa cipangano, cimene Yehova anacita nanu, kunena za mau awa onse,

9. Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akuru a Israyeli makumi asanu ndi awiri anakwerako;

10. ndipo anapenya Mulungu wa Israyeli; ndipo pansi pa mapazi ace panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiri, ndi ngati thupi la thambo loti mbe.

11. Koma sanaturutsa dzanja lace pa akuru a ena a Israyeli; ndipo anapenya Mulungu, nadya, namwa.

12. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi cilamulo ndi malamulo, ndawalembera kuti uwalangize.

13. Ndipo anauka Mose, ndi Yoswa mtumiki wace; ndipo Mose anakwera m'phiri la Mulungu.

Eksodo 24