Eksodo 24:15-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo Mose anakwera m'phirimo, ndi mtambo unaphimba phirilo,

16. Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe pa phiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri iye ali m'kati mwa mtambo anaitana Mose.

17. Ndipo maonekedwe a ulemerero wa Yehova anali ngati mota wonyeketsa pamwamba pa phiri, pamaso pa ana a Israyeli.

18. Ndipo Mose analowa m'kati mwa mtambo, nakwera m'phirimo; ndipo Mose anakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku.

Eksodo 24