Eksodo 23:31-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Ndipo ndidzalemba malire ako kuyambira ku Nyanja Yofiira, kufikira ku nyanja ya Afilisiti, ndi kuyambira kucipululu kufikira ku Nyanja; popeza ndidzapereka okhala m'dzikolo m'dzanja lako, ndipo uziwaingitsa pamaso pako.

32. Usapangana nao, kapena ndi milungu yao.

33. Asakhale m'dziko lako iwowa, kuti angakulakwitse pa loe; pakuti ukatumikira milungu yao, kudzakukhalira msampha ndithu.

Eksodo 23