1. Ndipo Mulungu ananena mau onse amenewa, nati:
2. INE ndine YEHOVA Mulungu wako, amene ndinaturutsa iwe ku dziko la Aigupto, ku nyumba ya akapolo.
3. Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha.
4. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciri conse ca zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko;