4. Ndipo mlongo wace anaima patali, adziwe comwe adzamcitira.
5. Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'nyanja; ndipo atsikana ace anayendayenda m'mbali mwa nyanja; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wace akatenge.
6. Pamene anakabvundukula, anapenya mwanayo; ndipo, taonani, khandalo lirikulira. Ndipo anamva naye cifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri.
7. Pamenepo mlongo wace ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo?
8. Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita. Napita namwaliyo, nakaitana amace wa mwanayo.