6. Masiku asanu ndi awiri uzikadya mkate wopanda cotupitsa, ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri likhale la madyerero a Yehova.
7. Azikadya mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiriwo ndipo kasaoneke kanthu ka cotupitsa kwanu; inde cotupitsa cisaoneke kwanu m'malire ako onse.
8. Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero cifukwa comwe Yehova anandicitira ine poturuka ine m'Aigupto,
9. Ndipo cizikhala ndi iwe ngati cizindikilo pa dzanja lako, ndi cikumbutso pakati pa maso ako; kuti cilamulo ca Yehova cikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakuturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu.
10. Cifukwa cace uzikasunga lemba ili pa nyengo yace caka ndi caka.