Eksodo 10:21-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kuthambo, ndipo padzakhala mdima pa dziko la Aigupto, ndiwo mdima wokhudzika.

22. Ndipo Mose anatambasulira dzanja lace kuthambo; ndipo munali mdima bii m'dziko lonse la Aigupto masiku atatu;

23. sanaonana, sanaukanso munthu pamalo pace, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israyeli kudayera m'nyumba zao.

24. Ndipo Farao anaitana Mose, nati, Mukani, tumikirani Yehova; nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu zokha zitsale; mumuke nao ana anu ang'ononso.

25. Koma Mose anati, Mutipatsenso m'dzanja mwathu nsembe zophera ndi nsembe zopsereza, kuti timkonzere Yehova Mulungu wathu.

26. Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; cosatsala ciboda cimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.

27. Koma Yehova analimbitsa mtima wace wa Farao, ndipo anakana kuwaleka amuke.

Eksodo 10