13. Pamenepo Mose analoza ndodo yace pa dziko la Aigupto; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutaca mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe.
14. Ndipo dzombe linakwera pa dziko lonse la Aigupto, ndipo linatera pakati pa malire onse a Aigupto, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.
15. Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m'dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsala cabiriwiri ciri conse, pamitengo kapena pa zitsamba za kuthengo, m'dziko lonse la Aigupto.
16. Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu.
17. Ndipo tsopano, ndikhululukirenitu kulakwa kwanga nthawi yino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andicotsere imfa yino yokha.