7. Ana a Israyeli ndipo anaswana, nabalana, nacuruka, nakhala nazo mphamvu zazikuru; ndipo dziko linadzala nao.
8. Pamenepo inalowa mfumu yatsopano m'ufumu wa Aigupto, imene siinadziwa Yosefe.
9. Ndipo ananena ndi anthu ace, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israyeli, acuruka, natiposa mphamvu.
10. Tiyeni, tiwacenjerere angacuruke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kucoka m'dzikomo.
11. Potero anawaikira akuru a misonkho kuti awasautse ndi akatunduno. Ndipo anammangira Farao midzi yosungiramo cuma, ndiyo Pitomu ndi Ramese.