11. Potero anawaikira akuru a misonkho kuti awasautse ndi akatunduno. Ndipo anammangira Farao midzi yosungiramo cuma, ndiyo Pitomu ndi Ramese.
12. Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anacuruka, momwemonso anafalikira. Ndipo anabvutika cifukwa ca ana a Israyeli.
13. Ndipo Aaigupto anawagwiritsa ana a Israyeli nchito yosautsa;
14. nawawitsa moyo wao ndi nchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi nchito zonse za pabwalo, nchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.
15. Ndipo mfumu ya Aigupto inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lace la wina ndiye Sifra, dzina la mnzace ndiye Puwa;
16. ninati, Pamene muciza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo.
17. Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanacita monga mfumu ya Aigupto inawauza, koma analeka ana amuna akhale ndi moyo.