3. Ndipo anakucepetsani, nakumvetsani odala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwa, angakhale makolo anu sanawadziwa; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakuturuka m'kamwa mwa Yehova.
4. Zobvala zanu sizinatha pathupi panu, phazi lanu silinatupa zaka izi makumi anai.
5. Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wace, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.
6. Ndipo muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace, ndi kumuopa.
7. Pakuti Yehova Mulungu wanu akulowetsani m'dziko lokoma, dziko la mitsinje yamadzi, la akasupe, ndi la maiwe akuturuka m'zigwa, ndi m'mapiri;